Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? |
Kodi Amakhulupirira Chiyani?A Mboni za Yehova amakhulupirira Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Zinthu za chilengedwe zodabwitsa kwambiri zotizinga zimaonetsa kuti chilengedwechi chinapangidwa ndi Mlengi wanzeru ndi wamphamvu kwambiri. Monga mmene ntchito za amuna ndi akazi zimaonetsera maluso awo, zimateronso ntchito za Yehova Mulungu. Baibulo limatiuza kuti “chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake . . . popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” Ndiponso, popanda mawu, “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 1:20; Salmo 19:1-4.
Anthu saumba mbiya kapena kupanga mawailesi akanema ndi makompyuta popanda cholinga. Dziko lapansi limodzi ndi zolengedwa zake, zomera ndi nyama n’zodabwitsa kwambiri kuposa zonsezo. Kapangidwe ka thupi la munthu limodzi ndi mamiliyoni mamiliyoni a maselo ake n’zosatheka ifeyo kuzimvetsa—ngakhale ubongo weniweniwo umene timaganiza nawo n’ngwodabwitsa moti sititha kuumvetsa! Ngati anthu amakhala ndi cholinga popanga zinthu zawo zosadabwitsa kwenikwenizo, kunena zoona Yehova Mulungu ayenera kuti anali ndi cholinga polenga zinthu zodabwitsazo! Miyambo 16:4 imati iye ali nacho cholinga mwakunena kuti: “Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zawo.”
Yehova anali ndi cholinga popanga dziko lapansi, monga momwe anauzira anthu aŵiri oyamba kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, . . . , mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Chifukwa chakuti anthu aŵiri oyambawo sanamvere, analephera kudzaza dziko lapansi ndi mabanja olungama amene akanasamalira bwino dziko lapansi limodzi ndi zomera ndi nyama zake. Koma kulephera kwawo sikunalepheretsenso cholinga cha Yehova. Patapita zaka zikwi zambirimbiri, olemba Mawu analemba kuti: “Mulungu amene anaumba dziko lapansi . . . , sanalilenga mwachabe.” Iye “analiumba akhalemo anthu.” Silidzawonongedwa, koma ‘dziko likhalabe masiku onse.’ (Yesaya 45:18; Mlaliki 1:4) Cholinga cha Yehova popanga dziko lapansi chidzakwaniritsidwa: “Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.”—Yesaya 46:10.
Chotero, Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti dziko lapansi lidzakhalapo ku nthaŵi zonse ndipo anthu onse, amoyo ndi akufa, amene adzayenerera cholinga cha Yehova chokhazikitsira dziko lapansi lokongola, adzakhalapo ndi moyo kosatha. Anthu onse analandira kupanda ungwiro kuchokera kwa Adamu ndi Hava, choncho onse ndi ochimwa. (Aroma 5:12) Baibulo limatiuza kuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa.” “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Aroma 6:23; Mlaliki 9:5; Ezekieli 18:4, 20) Koma ndi motani mmene iwo angakhalirenso ndi moyo ndi kulandira nawo madalitso a m’dziko lapansi? Ndi kokha mwa nsembe ya dipo la Kristu Yesu, pakuti iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” “Onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; 11:25; Mateyu 20:28. Kodi zimenezi zidzatheka motani? Zafotokozedwa mu “uthenga wabwino wa Ufumu,” umene Yesu anayamba kuulalikira pamene anali padziko lapansi. (Mateyu 4:17-23) Koma lerolino, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino m’njira yapadera kwambiri. | ||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||
ZIMENE A MBONI ZA YEHOVA AMAKHULUPIRIRA
| ||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||||
Kofalitsidwa mu 2000 |